5. Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;
6. akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita ku malo amodzi?
7. Nchito zace zonse munthu angogwirira m'kamwa mwace, koma mtima wace sukhuta.
8. Pakuti wanzeru ali ndi ciani coposa citsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pa maso pa amoyo ali ndi ciani?
9. Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
10. Comwe cinalipo cachedwa dzina lace kale, cidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.
11. Pokhala zinthu zambiri zingocurukitsa zacabe, kodi anthu aona phindu lanji?