2. Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa coipa canji cidzaoneka pansi pano.
3. Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwela pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.
4. Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.
5. Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa nchito za Mulungu amene acita zonse.
6. Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.
7. Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa.