Miyambi 9:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ukhala pa khomo la nyumba yace,Pampando pa misanje ya m'mudzi

15. Kuti uitane akupita panjira,Amene angonkabe m'kuyenda kwao,

16. Wacibwana ndani? Apambukire kuno.Ati kwa yense wopanda nzeru,

17. Madzi akuba atsekemera,Ndi cakudya cobisika cikoma.

18. Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko;Omwe acezetsa utsiru ali m'manda akuya.

Miyambi 9