Miyambi 5:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo tsopano ana, mundimvere,Musapatuke ku mau a m'kamwa mwanga.

8. Siyanitsa njira yako kutari kwa iyeyo,Osayandikira ku khomo la nyumba yace;

9. Kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,Ndi zaka zako kwa ankhanza;

10. Kuti mphamvu yako isakhutitse alendo,Ndi kuti usagwire nchito m'nyumba ya wacilendo;

11. Ungalire pa cimariziro cako,Pothera nyama yako ndi thupi lako;

12. Ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,Mtima wanga ndi kunyoza cidzudzulo;

Miyambi 5