Miyambi 3:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Usadziyese wekha wanzeru;Opa Yehova, nupatuke pazoipa;

8. Mitsempha yako idzalandirapo moyo,Ndi mafupa ako uwisi.

9. Lemekeza Yehova ndi cuma cako,Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;

10. Motero nkhokwe zako zidzangoti the,Mbiya zako zidzasefuka vinyo.

11. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova,Ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwace;

Miyambi 3