Miyambi 29:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Mfumu akhazikitsa dziko ndi ciweruzo;Koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa.

5. Wosyasyalika mnzace Acherera mapazi ace ukonde.

6. M'kulakwa kwa woipa muli msampha;Koma wolungama ayimba, nakondwera.

7. Wolungama asamalira mlandu wa osauka;Koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.

Miyambi 29