Miyambi 29:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Mkuru akamvera cinyengo,Atumuki ace onse ali oipa,

13. Waumphawi ndi wotsendereza akumana;Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo.

14. Mfumu yolamulira osauka mwantheradi,Mpando wace udzakhazikika kufikira nthawi zonse.

15. Ntyole ndi cidzudzulo zipatsa nzeru;Koma mwana womlekerera acititsa amace manyazi.

16. Pocuruka oipa zolakwa zicuruka;Koma olungama adzaona kugwa kwao.

Miyambi 29