Miyambi 28:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Waumphawi woyenda mwangwiroApambana ndi yemwe akhotetsa njira zace, angakhale alemera.

7. Wosunga cilamulo ndiye mwana wozindikira;Koma mnzao wa adyera acititsa atate wace manyazi.

8. Wocurukitsa cuma cace, pokongoletsa ndi phindu,Angokundikira yemwe acitira osauka cisoni.

9. Wopewetsa khutu lace kuti asamve cilamulo,Ngakhale pemphero lace linyansa.

10. Wosoceretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa,Adzagwa mwini m'dzenje lace;Koma angwiro adzalandira colowa cabwino.

11. Wolemera adziyesa wanzeru;Koma wosauka wozindikira aululitsa zace.

12. Posekera olungama pali ulemerero wambiri;Koma pouka oipa anthu amabisala.

13. Wobisa macimo ace sadzaona mwai;Koma wakuwabvomereza, nawasiya adzacitidwa cifundo.

14. Wodala munthu wakuopakosalekeza;Koma woumitsa mtima wace adzagwa m'zoipa.

15. Monga mkango wobangula ndi cirombo coyendayenda,Momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.

16. Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa;Koma yemwe ada cisiriro adzatanimphitsa moyo wace.

17. Woparamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje;Asamuletse.

Miyambi 28