Miyambi 21:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu;Koma yense wansontho angopeza umphawi.

6. Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

7. Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola;Cifukwa akana kucita ciweruzo.

8. Wosenza cimo njira yace ikhotakhota;Koma nchito ya woyera mtima ilungama.

9. Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.

10. Wamphulupulu mtima wace umkhumba zoipa;Sakomera mtima mnzace.

11. Polangidwa wonyoza, wacibwana alandira nzeru,Naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.

Miyambi 21