Miyambi 21:20-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;Koma wopusa angozimeza.

21. Wolondola cilungamo ndi cifundoApeza moyo, ndi cilungamo, ndi ulemu.

22. Wanzeru akwera pa mudzi wa olimba,Nagwetsa mphamvu yace imene anaikhulupirira.

23. Wosunga m'kamwa mwace ndi lilime laceAsunga moyo wace kumabvuto.

24. Wonyada wodzikuza dzina lace ndiye wonyoza;Acita mwaukali modzitama.

Miyambi 21