Miyambi 21:18-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Wocimwa ndiye ciombolo ca wolungama;Ndipo waciwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.

19. Kukhala m'cipululu kufunikaKuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.

20. Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;Koma wopusa angozimeza.

21. Wolondola cilungamo ndi cifundoApeza moyo, ndi cilungamo, ndi ulemu.

Miyambi 21