Miyambi 21:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mphatso ya m'tseri ipembedza mkwiyo,Ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.

15. Kucita ciweruzo kukondweretsa wolungama;Koma kuwaononga akucita mphulupulu,

16. Munthu wosocera pa njira ya nzeruAdzakhala m'msonkhano wa akufa.

17. Wokonda zoseketsa adzasauka;Wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

18. Wocimwa ndiye ciombolo ca wolungama;Ndipo waciwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.

19. Kukhala m'cipululu kufunikaKuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.

Miyambi 21