Miyambi 2:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwananga, ukalandira mau anga,Ndi kusunga malamulo anga;

2. Kucherera makutu ako kunzeru,Kulozetsa mtima wako kukuzindikira;

3. Ukaitananso luntha,Ndi kupfuulira kuti ukazindikire;

4. Ukaifunafuna ngati siliva,Ndi kuipwaira ngati cuma cobisika;

5. Pompo udzazindikira kuopa YehovaNdi kumdziwadi Mulungu.

6. Pakuti Yehova apatsa nzeru;Kudziwa ndi kuzindikira kuturuka m'kamwa mwace;

7. Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni;Ndiye cikopa ca oyenda molunjika;

8. Kuti acinjirize njira za ciweruzo,Nadikire khwalala la opatulidwa ace.

9. Pamenepo udzazindikira cilungamo ndi ciweruzo,Zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.

10. Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako,Moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,

Miyambi 2