22. Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace;Ndipo wosauka apambana munthu wonama.
23. Kuopa Yehova kupatsa moyo;Wokhala nako adzakhala wokhuta;Zoipa sizidzamgwera.
24. Wolesi alonga dzanja lace m'mbale,Osalibwezanso kukamwa kwace.
25. Menya wonyoza, ndipo acibwana adzaceniera;Nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.
26. Wolanda za atate, ndi wopitikitsa amai,Ndiye mwana wocititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.