Miyambi 17:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Kapolo wocitamwanzeruAdzalamulira mwana wocititsa manyazi,Nadzagawana nao abale colowa.

3. Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golidi ali ndi ng'anjo;Koma Yehova ayesa mitima.

4. Wocimwa amasamalira milomo yolakwa;Wonama amvera lilime losakaza.

5. Wocitira ciphwete aumphawi atonza Mlengi;Wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka cilango.

6. Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;Ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

7. Mlomo wangwiro suyenera citsiru;Ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.

Miyambi 17