15. Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama,Onse awiriwa amnyansa Yehova.
16. Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la citsiru,Popeza wopusa alibe mtima?
17. Bwenzi limakonda nthawi zonse;Ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.
18. Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,Napereka cikole pamaso pa mnzace.
19. Wokonda ndeu akonda kulakwa;Ndipo wotarikitsa khomo lace afunafuna kuonongeka.
20. Wokhota mtima sadzapeza bwinoNdipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.
21. Wobala citsiru adzicititsa cisoni;Ndipo atate wa wopusa sakondwa.
22. Mtima wosekerera uciritsa bwinoKoma mzimu wosweka uphwetsa mafupa,