Miyambi 17:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ciyambi ca ndeu cifanana ndi kutsegulira madzi;Tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.

15. Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama,Onse awiriwa amnyansa Yehova.

16. Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la citsiru,Popeza wopusa alibe mtima?

17. Bwenzi limakonda nthawi zonse;Ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.

18. Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,Napereka cikole pamaso pa mnzace.

Miyambi 17