Miyambi 16:7-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Njira za munthu zikakonda Yehova,Ayanjanitsana naye ngakhale adani ace.

8. Zapang'ono, pokhala cilungamo,Ziposa phindu lalikuru lopanda ciweruzo.

9. Mtima wa munthu ulingalira njira yace;Koma Yehova ayendetsa mapazi ace.

10. Mau a mlauli ali m'milomo ya mfumu;M'kamwa mwace simudzacita cetera poweruza.

11. Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova;Ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m'thumba.

12. Kucita mphulupulu kunyansa mafumu;Pakuti mpando wao wakhazikika ndi cilungamo.

13. Milomo yolungama ikondweretsa mafumu;Wonena zoongoka amkonda.

14. Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa;Wanzeru adzaukhulula.

15. M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo;Kukoma mtima kwace kunga mtambo wa mvula ya masika.

16. Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golidi,Kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?

17. Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;Wosunga njira yace acinjiriza moyo wace.

Miyambi 16