Miyambi 15:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.

15. Masiku onse a wosauka ali oipa;Koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.

16. Zapang'ono, ulikuopa Yehova,Zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso,

17. Kudya masamba, pali cikondano,Kuposa ng'ombe yonenepa pali udani.

18. Munthu wozaza aputa makani;Koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

Miyambi 15