Miyambi 10:22-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Madalitso a Yehova alemeretsa,Saonjezerapo cisoni.

23. Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa;Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.

24. Comwe woipa aciopa cidzamfikira;Koma comwe olungama acifuna cidzapatsidwa.

25. Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi;Koma olungama ndiwo maziko osatha.

26. Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.

Miyambi 10