Miyambi 1:29-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Cifukwa anada nzeru,Sanafuna kuopa Yehova;

30. Anakana uphungu wanga,Nanyoza kudzudzula kwanga konse;

31. Momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,Nadzakhuta zolingalira zao.

32. Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa acibwana kudzawapha;Ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.

33. Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,Nadzakhala phe osaopa zoipa,

Miyambi 1