Miyambi 1:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Mwananga, usayende nao m'njira;Letsa phazi lako ku mayendedwe ao;

16. Pakuti mapazi ao athamangira zoipa,Afulumira kukhetsa mwazi.

17. Pakuti kuchera msampha pamaso pa mbalame ndi cabe;

18. Ndipo awa abisalira mwazi wao wao, alalira miyoyo yao yao.

19. Mayendedwe a yense wopindula cuma monyenga ngotere;Cilanda moyo wa eni ace,

Miyambi 1