Mika 2:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzacoka.

7. Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? izi ndi nchito zace kodi? Mau anga samcitira zokoma kodi, iye amene ayenda coongoka?

8. Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula copfunda ku maraya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.

9. Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; mucotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha.

10. Nyamukani, cokani, pakuti popumula panu si pano ai; cifukwa ca udio Wakuononga ndi cionongeko cacikuru.

Mika 2