Mateyu 6:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako, nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.

7. Ndipo popemphera musabwereze-bwereze cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao.

8. Cifukwa cace inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye.

9. Cifukwa cace pempherani inu comweci:Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.

10. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano.

11. Mutipatse ife lero cakudya cathu calero.

Mateyu 6