Mateyu 6:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu.

13. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.

14. Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.

15. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.

Mateyu 6