Mateyu 5:33-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, 5 Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako:

34. koma Ine ndinena kwa inu, 6 Musalumbire konse, kapena kuchula Kumwamba, cifukwa kuli cimpando ca Mulungu;

35. 7 kapena kuchula dziko lapansi, cifukwa liri popondapo mapazi ace; kapena kuchula Yerusalemu, cifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikurukuru.

36. 8 Kapena usalumbire ku mutu wako, cifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi.

37. 9 Kama manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo coonjezedwa pa izo cicokera kwa woipayo.

38. Munamva kuti kunanenedwa, 10 Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:

39. koma ndinena kwa inu, 11 Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako Lamanja, umtembenuzire linanso.

40. Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso copfunda cako.

Mateyu 5