38. Pamenepo anapacika pamodzi ndi Iyeacifwamba awiri, mmodzi ku dzanja lamanja, ndi wina kulamanzere.
39. Ndipo anthu akupitirirapo 1 anamcitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao,
40. nati, Nanga 2 Iwe, wopasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; 3 ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.
41. Comweconso ansembe akuru, pamodzi ndi alembi ndi akuru anamcitira cipongwe, nati,
42. Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye Mfumu ya Ayuda; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.
43. 4 Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.
44. Ndiponso 5 acifwambawo opacikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi.
45. Ndipo 6 ora lacisanu ndi cimodzi panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai.
46. Ndipo poyandikira ora lacisanu ndi cinai, Yesu 7 anapfuula ndi mau akuru, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
47. Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya.
48. Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, 8 natenga cinkhupule, nacidzaza ndi vinyo wosasa, naciika pabango, namwetsa Iye.
49. Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa.
50. Ndipo Yesu, 9 pamene anapfuula ndi mau akuru, anapereka mzimu wace.
51. Ndipo onani, 10 cinsaru cocinga ca m'Kacisi cinang'ambika pakati, kucokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;
52. ndi Manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;
53. ndipo anaturuka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwace, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri.
54. Ndipo pamene mkuru wa asilikari, ndi iwo anali naye 11 akudikira Yesu, anaona cibvomezi, ndi zinthu zimene zinacitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyo ndiye Mwana wa Mulungu.