Mateyu 27:24-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndiribe kucimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.

25. Ndipo anthu onse anabvomereza, ndi kuti, Mwazi wace uli pa ife ndi pa ana athu.

26. Pomwepo iye anamasulira iwo Baraba, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampacike pamtanda.

27. Pomwepo asilikari a kazembe anamuka naye Yesu ku bwalo la mirandu, nasonkhanitsa kwa iye khamu lao lonse.

28. Ndipo anabvula malaya ace, nambveka malaya ofiira acifumu.

29. Ndipo analuka korona waminga, nambveka pamutu pace, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lace; ndipo anagwada pansi pamaso pace, namcitira cipongwe, nati, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda!

30. Namthira malobvu, natenga bango, nampanda Iye pamutu.

31. Ndipo pamene anatha kumcitira Iye cipongwe, anabvula malaya aja, nambveka Iye malaya ace, namtsogoza Iye kukampacika pamtanda.

32. Ndipo pakuturukapao anapeza munthu wa ku Kurene, dzina lace Simoni, namkangamiza iye kuti anyamule mtanda wace.

33. Ndipo pamene anadza kumalo dzina lace Golgota, ndiko kunena kuti, Malo-abade,

Mateyu 27