20. Koma ansembe akuru anapangira anthu kuti apemphe Baraba, koma kuti aononge Yesu.
21. Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Baraba.
22. Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzacita ciani ndi Yesu, wochedwa Kristu?