Mateyu 26:6-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,

7. anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa yaalabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatari, nawatsanulira pamutu pace, m'mene Iye analikukhala pacakudya.

8. Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Cifukwa ninji kuononga kumeneku?

Mateyu 26