8. Ndipo opusa anati kwa ocenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; cifukwa nyali zathu zirikuzima.
9. Koma ocenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.
10. Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo, analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.