Mateyu 24:6-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.

7. Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m'malo akuti akuti.

8. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.

Mateyu 24