48. Koma kapolo woipa akanena mumtima mwace, Mbuye wanga wacedwa;
49. nadzayamba kupanda akapolo anzace, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera;
50. mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye,
51. nadzamdula, nadzaika pokhala pace ndi anthu onyenga; 8 pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.