Mateyu 24:19-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m'masiku awo!

20. Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yacisanu, kapena pa Sabata;

21. pakuti pomwepo padzakhala masauko akuru, monga sipadakhale otero kuyambira ciyambi ca dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.

22. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense: koma cifukwa ca osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.

23. Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Kristu ali kuno, kapena uko musambvomereze;

24. cifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.

25. Cifukwa cace akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'cipululu; musamukeko.

26. Onani, ali m'zipinda; musabvomereze.

27. Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwace kwa Mwana wa munthu.

28. Kumene kuli konse uli mtembo, miimba Idzasonkhanira konko.

29. Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwace, ndi nyenyezi zidzagwa kucokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:

30. ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo cizindikiro ca Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pacifuwa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.

31. Ndipo Iye adzatumiza angelo ace ndi kulira kwakukuru kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ace ku mphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ace ena.

32. Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene tsopano nthambi yace iri yanthete, nipuka masa-i mba ace, muzindikira kuti dzinja liyandikira;

33. comweconso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.

34. Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kucoka, kufikira zinthu zonsezi zidzacitidwa.

35. Thambo ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mau anga sadzacoka ai.

36. Koma za tsiku ilo ndi nthawi yace sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.

Mateyu 24