17. iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwace;
18. ndi iye wa m'munda asabwere kutenga copfunda cace.
19. Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m'masiku awo!
20. Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yacisanu, kapena pa Sabata;
21. pakuti pomwepo padzakhala masauko akuru, monga sipadakhale otero kuyambira ciyambi ca dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.
22. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense: koma cifukwa ca osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.
23. Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Kristu ali kuno, kapena uko musambvomereze;
24. cifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
25. Cifukwa cace akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'cipululu; musamukeko.
26. Onani, ali m'zipinda; musabvomereze.
27. Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwace kwa Mwana wa munthu.
28. Kumene kuli konse uli mtembo, miimba Idzasonkhanira konko.