Mateyu 23:7-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. ndi kulankhulidwa m'misika, ndi kuchedwa ndi anthu, Rabi.

8. Koma inu musachedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.

9. Ndipo inu musachule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.

10. Ndipo musachedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.

11. Koma wamkuru wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.

12. Ndipo amene ali yense akadzikuza yekha adzacepetsedwa; koma amene adzicepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

13. Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, Ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo. [

14. ]

15. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri.

16. Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene ali yense akalumbira kuchula Kacisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula golidi wa Kacisi, wadzimangirira.

17. Inu opusa, ndi akhungu: pakuti coposa nciti, golidi kodi, kapena Kacisi amene ayeretsa golidiyo?

18. Ndiponso, Amene ali yense akalumbira kuchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula mtulo wa pamwamba pace wadzimangirira.

19. Inu akhungu, pakuti coposa nciti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?

20. Cifukwa cace wakulumbira kuchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pace.

21. Ndipo wakulumbira kuchula Kacisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo.

22. Ndipo wakulumbira kuchula Kumwamba, alumbira cimpando ca Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.

Mateyu 23