1. Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anaturuka mamawa kuka lembera anchito a m'munda wace wampesa.
2. Ndipo parnene adapangana ndi anchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza ku munda wace.
3. Ndipo anaturuka dzuwa litakwera, naona ena ataima cabe pabwalo;
4. ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani cimene ciri coyenera. Ndipo iwo anapita.
5. Ndiponso anaturuka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nacita cimodzimodzi.
6. Ndipo poyandikira madzulo anaturuka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse cabe?
7. Iwo ananena kwa iye, Cifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso ku mundawo wampesa.