Mateyu 2:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Herode mfumuyo pakumva ici anabvutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.

4. Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe akuru onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Kristuyo?

5. Ndipo anamuuza iye, M'Betelehemu wa Yudeya; cifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,

6. Ndipo iwe: Betelehemu, dziko la Yudeya,Sukhala konse wamng'onong'ono mwa akuru a Yudeya.Pakuti Wotsogolera adzacokera mwaiwe,Amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.

7. Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yace idaoneka nyenyeziyo.

8. Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.

9. Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza niima pamwamba pomwe panali kamwanako.

Mateyu 2