21. Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amace, nalowa m'dziko la Israyeli.
22. Koma pakumva iye kuti Arikelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wace Herode, anacita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anacenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa ku dziko la Galileya,
23. nadza nakhazikika m'mudzi dzina lace Nazarete kuti cikacitidwe conenedwa ndi aneneri kuti, Adzachedwa Mnazarayo.