1. Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anacokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordano.
2. Ndipo makamu akuru a anthu anamtsata; ndipo Iye anawaciritsa kumeneko.
3. Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace pa cifukwa ciri conse?
4. Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu paciyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,
5. nati, Cifukwa ca ici mwamuna adzasiya atate wace ndi amace, nadzaphatikizana ndi mkazi wace, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?
6. cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Cifukwa cace ici cimene Mulungu anacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.