Mateyu 18:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

4. Cifukwa cace yense amene adzicepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.

5. Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka cifukwa ca dzina langa, alandira Ine;

6. koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikuru ikolowekedwe m'khosi mwace, namizidwe poya pa nyanja.

7. Tsoka liri hdi dziko lapansi cifukwa ca zokhumudwitsa! pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka liri ndi munthu amene cokhumudwitsaco cidza ndi iye.

8. Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m'moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri.

Mateyu 18