Mateyu 17:20-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Iye ananena kwa iwo, Cifukwa cikhulupiriro canu ncacing'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala naco cikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosacitika. [

21. ]

22. Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;

Mateyu 17