Mateyu 15:29-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo Yesu anacoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.

30. Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ace: ndipo Iye anawaciritsa;

31. kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nacira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.

32. Ndipo Yesu anaitana ophunzira ace, nati, Mtima wanga ucitira cifundo khamu la anthuwa, pakuti ali cikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira,

Mateyu 15