Mateyu 15:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ocokera ku Yerusalemu, nati,

2. Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? pakuti sasamba manja pakudya.

3. Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu cifukwa ca miyambo yanu?

Mateyu 15