14. Ndipo Afarisi anaturuka, nakhala upo womcitira Iye mwa kumuononga.
15. Koma Yesu m'mene anadziwa, anacokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawaciritsa iwo onse,
16. nawalimbitsira mau kuti asamuulule Iye;
17. kuti cikacitidwe conenedwa ndi Yesaya mneneri uja, kuti,
18. Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha,Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye;Pa Iye ndidzaika Mzimu wanga,Ndipo Iye adzalalikira ciweruzo kwa akunja.
19. Sadzalimbana, sadzapfuula;Ngakhale mmodzi sadzamva mau ace m'makwalala;
20. Bango lophwanyika sadzalityola,Ndi nyali yofuka sadzaizima,Kufikira Iye adzatumiza ciweruzo cikagonjetse,
21. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lace.