Mateyu 11:6-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo wodala iye amene sakhumudwa cifukwa ca Ine.

7. Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena Ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munaturuka kunka kucipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka nd: mphepo kodi?

8. Koma munaturuka kukaona ciani? Munthu wobvala zofewa kodi? Onani, akubvala zofewa alim'nyumba zamafumu.

9. Koma munaturukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri.

10. Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti,Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu,Amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.

11. Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.

12. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.

13. Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane.

14. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.

15. Amene ali ndi makutu akumva, amve.

16. Koma ndidzafanizira ndi ciani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao,

17. ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunabvina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira.

18. Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi ciwanda.

19. Mwana wa munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ocimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi nchito zace.

20. Pomwepo Iye anayamba kutonza midziyo, m'mene zinacitidwa zambiri za nchito zamphamvu zace, cifukwa kuti siinatembenuke.

21. Tsoka kwa iwe, Korazini! tsoka kwa iwe, Betsaida! cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa inu zikadacitidwa m'Turo ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kale kale m'ziguduli ndi m'phulusa.

Mateyu 11