Mateyu 11:3-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?

4. Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona:

5. akhungu alandira kuona kwao, Ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, indi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino.

6. Ndipo wodala iye amene sakhumudwa cifukwa ca Ine.

7. Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena Ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munaturuka kunka kucipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka nd: mphepo kodi?

8. Koma munaturuka kukaona ciani? Munthu wobvala zofewa kodi? Onani, akubvala zofewa alim'nyumba zamafumu.

9. Koma munaturukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri.

10. Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti,Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu,Amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.

11. Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.

12. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.

13. Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane.

14. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.

15. Amene ali ndi makutu akumva, amve.

16. Koma ndidzafanizira ndi ciani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao,

17. ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunabvina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira.

18. Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi ciwanda.

Mateyu 11