Mateyu 1:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ico colandiridwa mwa iye ciri ca Mzimu Woyera.

21. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao.

22. Ndipo zonsezi zinakhala kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,

23. Onani namwali adzaima,Nadzabala mwana wamwamuna,Ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli;ndilo losandulika, Mulungu nafe.

Mateyu 1