Masalmo 94:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Wodala munthu amene mumlanga, Yehova;Ndi kumphunzitsa m'cilamulo canu;

13. Kuti mumpumitse masiku oipa;Kufikira atakumbira woipa mbuna.

14. Pakuti Yehova sadzasiya anthu ace,Ndipo sadzataya colandira cace.

15. Pakuti ciweruzo cidzabwera kumka kucilungamo:Ndipo oongoka mtima onse adzacitsata.

16. Adzandiukira ndani kutsutsana nao ocita zoipa?Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ocita zopanda pace?

17. Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova,Moyo wanga ukadakhala kuli cete.

Masalmo 94