6. Munandiika kunsi kwa dzenje,Kuti mdima, kozama.
7. Mkwiyo wanu utsamira pa ine,Ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.
8. Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;Munandiika ndiwakhalire conyansa:Ananditsekereza osakhoza kuturuka ine.
9. Diso langa lapuwala cifukwa ca kuzunzika kwanga:Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;Nditambalitsira manja anga kwa Inu.
10. Kodi mudzacitira akufa zodabwiza?Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?
11. Adzafotokozera cifundo canu kumanda kodi,Cikhulupiriko canu ku malo a cionongeko?